-
Numeri 7:13-17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli* 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.*+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 14 Anaperekanso kapu imodzi* yagolide yolemera masekeli 10, yodzaza ndi zofukiza. 15 Komanso anapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 16 Anaperekanso mbuzi yaingʼono imodzi kuti ikhale ya nsembe yamachimo.+ 17 Iye anapereka ngʼombe ziwiri, nkhosa 5 zamphongo, mbuzi 5 zamphongo, ndi ana a nkhosa 5 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yamgwirizano.+ Izi nʼzimene Naasoni, mwana wa Aminadabu+ anapereka.
-