-
Genesis 12:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Yehova anauza Abulamu kuti: “Samuka mʼdziko lako ndi kuchoka pakati pa abale ako ndipo usiye nyumba ya bambo ako. Upite kudziko limene ndidzakuonetse.+ 2 Ndidzakupangitsa kuti ukhale mtundu waukulu. Ndidzakudalitsa ndipo ndidzapangitsa kuti dzina lako litchuke. Komanso anthu ena adzadalitsidwa chifukwa cha iwe.+ 3 Odalitsa iwe ndidzawadalitsa, ndipo wotemberera iwe ndidzamutemberera.+ Mabanja onse apadziko lapansi adzadalitsidwa* kudzera mwa iwe.”+
-