Ekisodo 28:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Udzaike Urimu ndi Tumimu*+ mʼchovala pachifuwa chachiweruzo, ndipo zizikhala pamtima pa Aroni akamakaonekera pamaso pa Yehova. Aroni azinyamula pamtima pake zinthu zogwiritsa ntchito poweruza Aisiraeli akamaonekera kwa Yehova nthawi zonse. Levitiko 8:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Choncho Mose anaitana Aroni ndi ana ake nʼkuwasambitsa ndi madzi.+ Levitiko 8:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Kenako anamuveka chovala chapachifuwa+ nʼkuika Urimu ndi Tumimu+ mʼchovala chapachifuwacho.
30 Udzaike Urimu ndi Tumimu*+ mʼchovala pachifuwa chachiweruzo, ndipo zizikhala pamtima pa Aroni akamakaonekera pamaso pa Yehova. Aroni azinyamula pamtima pake zinthu zogwiritsa ntchito poweruza Aisiraeli akamaonekera kwa Yehova nthawi zonse.