-
Deuteronomo 17:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Ngati mu umodzi mwa mizinda yanu muli mlandu wovuta kwambiri kuweruza kaya ndi mlandu wokhudza kukhetsa magazi,+ mlandu umene munthu wakasuma, mlandu wokhudza zachiwawa kapena mkangano, muzinyamuka nʼkupita kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.+ 9 Muzipita kwa Alevi omwe ndi ansembe ndi kwa woweruza+ amene akutumikira mʼmasiku amenewo. Muziwafotokozera nkhaniyo ndipo iwo azikuuzani chigamulo.+
-