26 Ukalanda mnzako chovala chake monga chikole cha ngongole,+ uzimubwezera dzuwa likamalowa. 27 Chifukwa chofunda chake nʼchomwecho. Ndi nsalu imene amafunda.+ Nanga afunda chiyani pogona? Ndiyeno akandilirira, ine ndidzamva ndithu, chifukwa ndine wachifundo.+