-
Yoswa 12:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Sihoni+ mfumu ya Aamori, yemwe ankakhala ku Hesiboni ndipo ankalamulira kuyambira kumzinda wa Aroweli,+ womwe unali mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni+ komanso kuyambira pakatikati pa chigwachi, ndi hafu ya Giliyadi mpaka kukafika kuchigwa cha Yaboki, kumalire ndi Aamoni. 3 Ankalamuliranso ku Araba mpaka kunyanja ya Kinereti*+ chakumʼmawa kwa nyanjayi, mpaka kukafika kunyanja ya Araba, yomwe ndi Nyanja Yamchere.* Komanso ankalamulira kumʼmawa, cha ku Beti-yesimoti ndiponso chakumʼmwera, kumunsi kwa Pisiga.+
-