-
Deuteronomo 3:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Pa nthawi imeneyo tinatenga dzikoli kukhala lathu kuchokera ku Aroweli,+ mzinda umene uli mʼchigwa cha Arinoni* ndi hafu ya dera lamapiri la Giliyadi. Ndipo ndinapereka mizinda yake kwa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi.+ 13 Mbali yotsala ya dera la Giliyadi ndi Basana yense amene anali mu ufumu wa Ogi ndinaipereka kwa hafu ya fuko la Manase.+ Dera lonse la Arigobi, limene ndi mbali ya Basana linkadziwika kuti ndi dziko la Arefai.
-