29 Mfumu ya Ai anaipachika pamtengo mpaka madzulo. Koma dzuwa litatsala pangʼono kulowa, Yoswa analamula kuti achotse mtembo wa mfumuyo pamtengopo.+ Atauchotsa anakauponya pageti la mzindawo nʼkuunjikapo mulu waukulu wa miyala, ndipo muluwo ulipo mpaka lero.