-
Yoswa 1:3-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Malo alionse amene phazi lanu lidzapondapo ndidzakupatsani, mogwirizana ndi zimene ndinalonjeza Mose.+ 4 Dziko lanu lidzayambira kuchipululu kufika ku Lebanoni mpaka kumtsinje waukulu wa Firate, dziko lonse la Ahiti+ mpaka kukafika ku Nyanja Yaikulu* kumadzulo.+ 5 Palibe amene adzakugonjetse masiku onse a moyo wako.+ Ndidzakhala nawe ngati mmene ndinakhalira ndi Mose+ ndipo sindidzakutaya kapena kukusiya.+
-