-
Genesis 18:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Choncho Abulahamu anathamangira kutenti kumene kunali Sara nʼkumuuza kuti: “Fulumira! Tenga ufa wosalala wokwana miyezo itatu,* uukande nʼkupanga mikate.” 7 Kenako Abulahamu anathamangira kumene kunali ziweto, nʼkusankha ngʼombe yaingʼono yamphongo yabwino kwambiri. Atatero, anaipereka kwa mtumiki wake, ndipo iye anaikonza mwamsanga.
-
-
Genesis 19:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ndiyeno Loti anawaumiriza kwambiri moti iwo anapita naye kunyumba kwake. Kumeneko anawakonzera phwando, nʼkuwaphikira mkate wopanda zofufumitsa, ndipo anadya.
-