36 Choncho ana a Loti awiri onsewo anakhala oyembekezera atagona ndi bambo awo. 37 Mwana woyamba anabereka mwana wamwamuna nʼkumupatsa dzina lakuti Mowabu.+ Iye ndi tate wa Amowabu amasiku ano.+
9 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti, ‘Usalimbane ndi Amowabu kapena kuchita nawo nkhondo, chifukwa sindidzakupatsa mbali iliyonse ya dziko lawo kuti likhale lako. Ndinapereka Ari kwa mbadwa za Loti+ kuti akhale malo awo.