-
Rute 2:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Boazi anamuyankha kuti: “Ndamva zonse zimene wachitira apongozi ako kuchokera pamene mwamuna wako anamwalira. Ndamvanso kuti unasiya bambo ako ndi mayi ako komanso dziko lakwanu, nʼkubwera kuno kwa anthu osawadziwa.+ 12 Yehova akupatse mphoto chifukwa cha zimene wachita,+ ndipo Yehova, Mulungu wa Isiraeli akulipire mokwanira* popeza wathawira mʼmapiko mwake kuti upeze chitetezo.”+
-