-
1 Mbiri 10:8-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Tsiku lotsatira, Afilisiti atabwera kudzatenga zinthu za anthu amene anaphedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atafa paphiri la Giliboa.+ 9 Iwo anamuvula Sauli zida zake nʼkumudula mutu. Kenako anauza anthu mʼdziko lonse la Afilisiti kuti afalitse uthengawu kwa mafano awo+ ndiponso kwa anthu onse. 10 Kenako anakaika zida zakezo mʼnyumba* ya mulungu wawo ndipo mutu wake anaumangirira kunyumba ya Dagoni.+
-