-
1 Samueli 2:14-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Akatero ankapisa folokoyo mʼbeseni, mʼpoto wa zogwirira ziwiri, mumphika kapena mʼpoto wa chogwirira chimodzi. Ndiyeno wansembe ankatenga chilichonse chimene folokoyo yatulutsa. Zimenezi ndi zimene ankachitira Aisiraeli onse opita ku Silo. 15 Komanso munthu wopereka nsembe asanapsereze mafuta,+ mtumiki wa wansembe ankabwera nʼkumuuza kuti: “Ndipatse nyama yosaphika ndikawotchere wansembe. Wansembe sakufuna nyama yophika koma yosaphika.” 16 Munthuyo akanena kuti: “Yembekeza kaye apsereze mafutawo+ kenako utenge chilichonse chimene ukufuna,” iye ankayankha kuti: “Ayi, ndipatse pompano, apo ayi ndichita kulanda!”
-