-
Yesaya 31:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Chifukwa izi ndi zimene Yehova wandiuza:
“Mkango umalira moopseza, mkango wamphamvu umalira poteteza nyama imene wagwira.
Abusa ambirimbiri akaitanidwa kuti adzauthamangitse,
Suchita mantha ukamva mawu awo
Kapena kutekeseka chifukwa cha phokoso lawo.
Mofanana ndi zimenezi, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzatsika kuti achite nkhondo
Poteteza phiri la Ziyoni ndiponso poteteza phiri lake lalingʼono.
-