-
1 Mafumu 2:29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Kenako Mfumu Solomo inauzidwa kuti: “Yowabu wathawira kuchihema cha Yehova ndipo ali pambali pa guwa lansembe.” Choncho Solomo anatuma Benaya mwana wa Yehoyada kuti: “Pita ukamuphe!”
-
-
1 Mbiri 27:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Mtsogoleri wa gulu lachitatu, lotumikira mwezi wachitatu, anali Benaya+ mwana wa Yehoyada+ wansembe wamkulu. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 6 Benaya ameneyu anali mwamuna wamphamvu pa amuna 30 komanso anali mtsogoleri wa amuna 30 amenewo. Pagulu lakelo, mwana wake Amizabadi ndi amene anali mtsogoleri.
-