-
1 Mbiri 22:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Tamvera, udzabereka mwana.+ Mwana ameneyo adzakhala munthu wokonda mtendere ndipo ndidzachititsa kuti azikhala mwamtendere komanso asamavutitsidwe ndi adani ake omuzungulira.+ Nʼchifukwa chake dzina lake adzakhala Solomo*+ ndipo mʼmasiku ake ndidzapatsa Aisiraeli bata ndi mtendere.+ 10 Iyeyo ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.+ Adzakhala mwana wanga ndipo ine ndidzakhala bambo ake.+ Ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mu Isiraeli ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.’+
-