-
Deuteronomo 12:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Mʼmalomwake, mudzafunefune Yehova Mulungu wanu pamalo alionse amene adzasankhe kuti aikepo dzina lake komanso malo amene azidzakhala pakati pa mafuko anu onse, ndipo muzidzapita kumeneko.+ 6 Nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,*+ chopereka chochokera mʼmanja mwanu,+ nsembe zimene mukupereka pokwaniritsa lonjezo, nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ngʼombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzapita nazo kumalo amenewo.+
-
-
1 Mafumu 8:28, 29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Inu Yehova Mulungu wanga, mumvetsere pemphero la mtumiki wanu ndi pempho lake lopempha chifundo. Imvani kulira kwanga kopempha thandizo komanso pemphero limene ine mtumiki wanu ndikupemphera kwa inu lero. 29 Maso anu akhale akuyangʼana nyumba ino masana komanso usiku. Akhale akuyangʼana malo amene munanena kuti, ‘Dzina langa lidzakhala kumeneko,’+ kuti mumvetsere pemphero limene mtumiki wanu angapemphere atayangʼana kumalo ano.+
-