1 Mafumu 9:27, 28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Mʼzombomo, Hiramu ankatumizamo antchito ake odziwa bwino zapanyanja+ kuti akagwire ntchito limodzi ndi antchito a Solomo. 28 Iwo ankapita ku Ofiri+ nʼkukatenga golide wokwana matalente 420 nʼkubwera naye kwa Mfumu Solomo. Salimo 45:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Ana aakazi a mafumu ali mʼgulu la akazi amene umawalemekeza. Mkazi wamkulu wa mfumu waima* kudzanja lako lamanja atavala zovala zagolide wa ku Ofiri.+
27 Mʼzombomo, Hiramu ankatumizamo antchito ake odziwa bwino zapanyanja+ kuti akagwire ntchito limodzi ndi antchito a Solomo. 28 Iwo ankapita ku Ofiri+ nʼkukatenga golide wokwana matalente 420 nʼkubwera naye kwa Mfumu Solomo.
9 Ana aakazi a mafumu ali mʼgulu la akazi amene umawalemekeza. Mkazi wamkulu wa mfumu waima* kudzanja lako lamanja atavala zovala zagolide wa ku Ofiri.+