-
1 Mafumu 12:28-30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Mfumuyo itakambirana ndi anthu ena inapanga ana awiri a ngʼombe agolide,+ kenako inauza anthu onse kuti: “Ndikuona kuti mukuvutika kwambiri kupita ku Yerusalemu. Ndiye ndakupangirani Mulungu uyu, amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo+ Aisiraeli inu.” 29 Choncho mwana wa ngʼombe wina anamuika ku Beteli+ ndipo wina anakamuika ku Dani.+ 30 Zimenezi zinachititsa kuti anthuwo achimwe+ ndipo iwo ankakafika mpaka ku Dani kukalambira mwana wa ngʼombeyo.
-
-
1 Mafumu 13:33, 34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Ngakhale kuti zimenezi zinachitika, Yerobowamu sanasiye kuchita zoipa. Iye anapitiriza kuika anthu wamba kuti akhale ansembe a malo okwezeka.+ Aliyense wofuna unsembewo, iye ankamʼpatsa ponena kuti: “Uyu akhale wansembe wa malo okwezeka.”+ 34 Tchimo la nyumba ya Yerobowamuli,+ linachititsa kuti anthu onse amʼnyumba yake awonongedwe nʼkufafanizidwa padziko lapansi.+
-