-
2 Mbiri 12:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Mʼchaka cha 5 cha Mfumu Rehobowamu, Sisaki+ mfumu ya Iguputo anabwera kudzaukira Yerusalemu, chifukwa iwo anachita zosakhulupirika kwa Yehova. 3 Anabwera kuchokera ku Iguputo ndi magaleta 1,200, amuna okwera pamahatchi 60,000 komanso anthu osawerengeka. Anthuwo anali Alibiya, Asuki ndi Aitiyopiya.+ 4 Sisakiyo analanda mizinda ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo kenako anafika ku Yerusalemu.
-