-
1 Mafumu 15:25-29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Nadabu+ mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Isiraeli mʼchaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo analamulira Isiraeli zaka ziwiri. 26 Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo anatsatira njira ya bambo ake+ komanso machimo amene Aisiraeli anachita chifukwa cha bambo akewo.+ 27 Ndiyeno Basa mwana wa Ahiya wa nyumba ya Isakara, anakonzera chiwembu Nadabu ndipo anamupha mumzinda wa Gibitoni,+ womwe unali mʼmanja mwa Afilisiti. Anamupha pa nthawi imene Nadabuyo ndi Aisiraeli onse ankaukira Gibitoni. 28 Basa anapha Nadabu mʼchaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda ndipo anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 29 Basa atangokhala mfumu, anapha anthu onse a mʼnyumba ya Yerobowamu. Sanasiye munthu aliyense wa mʼbanja la Yerobowamu ali ndi moyo. Anapha onse mogwirizana ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa mtumiki wake Ahiya wa ku Silo.+
-