-
2 Mbiri 18:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Kenako Yehosafati anafunsa kuti: “Kodi kuno kulibe mneneri wina wa Yehova?+ Ngati alipo, tiyeni tifunsirenso kwa Mulungu kudzera mwa iyeyo.”+ 7 Mfumu ya Isiraeli inayankha Yehosafati kuti: “Patsala munthu mmodzi+ amene tingathe kufunsira kwa Yehova kudzera mwa iye, koma ndimadana naye kwambiri, chifukwa salosera zabwino zokhudza ine, koma zoipa zokhazokha.+ Dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.” Koma Yehosafati anati: “Mfumu siyenera kulankhula choncho.”
-