9 Chifukwa iwo ndi anthu opanduka,+ ana ochita zachinyengo,+
Ana amene safuna kumva malamulo a Yehova,+
10 Iwo auza anthu oona masomphenya kuti, ‘Lekani kuona masomphenya,’
Ndipo anthu olosera zamʼtsogolo awauza kuti, ‘Musatiuze masomphenya olondola.+
Mutiuze zinthu zotikomera. Muziona masomphenya abodza.+