-
2 Mafumu 12:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Zitatero Yehoasi mfumu ya Yuda anatenga zopereka zonse zopatulika zimene makolo ake Yehosafati, Yehoramu ndi Ahaziya, mafumu a Yuda anaziyeretsa. Anatenganso zopereka za iyeyo zopatulika, ndi golide yense yemwe anali mosungira chuma cha mʼnyumba ya Yehova ndi cha mʼnyumba ya mfumu nʼkuzitumiza kwa Hazaeli mfumu ya Siriya.+ Choncho Hazaeli anabwerera osaukira Yerusalemu.
-
-
2 Mbiri 16:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Zitatero, Asa anatenga siliva ndi golide pa chuma chamʼnyumba ya Yehova+ ndi chamʼnyumba ya mfumu nʼkutumiza kwa Beni-hadadi mfumu ya Siriya,+ amene ankakhala ku Damasiko, ndi uthenga wakuti: 3 “Pali pangano pakati pa ine ndi iwe ndiponso pakati pa bambo anga ndi bambo ako. Ndakutumizira siliva ndi golide. Bwera udzaphwanye pangano lako ndi Basa mfumu ya Isiraeli kuti achoke mʼdera langa.”
-