30 Yehova wanena kuti: “Tsoka kwa ana aamuna osamvera,+
Amene amachita zofuna zawo osati zofuna zanga,+
Amene amapanga mgwirizano koma osati motsogoleredwa ndi mzimu wanga,
Kuti awonjezere tchimo pa tchimo.
2 Iwo amapita ku Iguputo+ asanandifunse,+
Kuti akapeze chitetezo kwa Farao
Ndiponso kuti akabisale mumthunzi wa Iguputo.