18 Inu Mulungu wanga, tcherani khutu lanu kuti mumve. Tsegulani maso anu kuti muone zimene zatichitikira komanso mmene mzinda wodziwika ndi dzina lanu wawonongekera. Ifeyo sitikukuchondererani chifukwa choti tachita zinthu zolungama ayi, koma chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+