-
2 Mafumu 24:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Yehoyakini mfumu ya Yuda anapita kwa mfumu ya Babulo+ pamodzi ndi mayi ake, atumiki ake, akalonga ake ndi nduna za panyumba yake+ ndipo mfumu ya Babuloyo inamutenga nʼkupita naye ku ukapolo mʼchaka cha 8 cha ufumu wake.+ 13 Mfumu ya Babulo inatenga chuma chonse cha mʼnyumba ya Yehova ndi chuma cha mʼnyumba ya mfumu.+ Inaphwanyaphwanyanso ziwiya zonse zagolide zimene Solomo mfumu ya Isiraeli anapanga kuti zikhale za mʼkachisi wa Yehova.+ Zimenezi zinachitika mogwirizana ndi zimene Yehova analosera.
-
-
Yeremiya 27:21, 22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena zokhudza ziwiya zimene zinatsala mʼnyumba ya Yehova, mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndi zimene zinatsala ku Yerusalemu kuti: 22 ‘“Ziwiya zimenezi zidzapita ku Babulo+ ndipo zidzakhala kumeneko mpaka tsiku limene ndidzazikumbukire,” akutero Yehova. “Ndipo ndidzazitenga nʼkuzibwezeretsa pamalo ano.”’”+
-