-
1 Mafumu 8:63, 64Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
63 Solomo anapereka nsembe zamgwirizano+ kwa Yehova. Anapereka ngʼombe 22,000 ndi nkhosa 120,000. Choncho mfumuyo ndi Aisiraeli onse anatsegulira nyumba ya Yehova.+ 64 Tsiku limenelo, mfumu inapatula pakati pa bwalo la nyumba ya Yehova chifukwa inkafunika kuperekerapo nsembe zopsereza, nsembe zambewu komanso mafuta a nsembe zamgwirizano. Inachita zimenezi chifukwa guwa lansembe lakopa*+ lapatsogolo pa kachisi wa Yehova linali lalingʼono kwambiri moti nsembe zopsereza, nsembe zambewu ndiponso mafuta+ a nsembe zamgwirizano sizikanakwanapo.
-