-
Yoswa 15:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Ichi chinali cholowa cha fuko la Yuda, motsatira mabanja awo.
-
-
1 Samueli 27:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Kenako Davide anauza Akisi kuti: “Ngati mungandikomere mtima, ndimapempha kuti andipatseko malo mumzinda umodzi wakutali kuti ndikakhale kumeneko. Palibe chifukwa choti ine mtumiki wanu ndizikhala limodzi ndi inu mumzinda wachifumu.” 6 Choncho pa tsikuli Akisi anapatsa Davide mzinda wa Zikilaga.+ Nʼchifukwa chake mzinda wa Zikilaga ndi wa mafumu a Yuda mpaka lero.
-