-
2 Samueli 6:17-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Kenako anaika Likasa la Yehova pamalo ake mutenti imene Davide anamanga.+ Ndiyeno Davide anapereka kwa Yehova+ nsembe zopsereza+ ndi nsembe zamgwirizano.+ 18 Davide atamaliza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano, anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 19 Komanso anapatsa anthu onse mikate yozungulira yoboola pakati, makeke a zipatso za kanjedza ndi makeke a mphesa. Anapereka zimenezi ku gulu lonse la Isiraeli, mwamuna ndiponso mkazi. Kenako aliyense anapita kunyumba kwake.
-