-
2 Samueli 24:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Yehova anakwiyiranso kwambiri Aisiraeli+ pamene winawake anaukira Aisiraeli nʼkuuza Davide kuti: “Pitani mukawerenge+ anthu a Isiraeli ndi Yuda.”+ 2 Choncho mfumu inauza Yowabu+ mkulu wa magulu ankhondo amene anali naye kuti: “Upite mʼmafuko onse a Isiraeli kuyambira ku Dani mpaka ku Beere-seba+ ndipo ukawerenge anthu kuti ndidziwe chiwerengero chawo.” 3 Koma Yowabu anauza mfumu kuti: “Yehova Mulungu wanu awonjezere anthu kuwirikiza ka 100 ndipo inu mbuyanga mfumu muone zimenezi zikuchitika. Koma nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchita zimenezi mbuyanga mfumu?”
-