-
1 Mbiri 29:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Ine ndayesetsa mwakhama kukonzekera nyumba ya Mulungu wanga. Ndapereka golide wodzapangira zinthu zagolide, siliva wodzapangira zinthu zasiliva, kopa* wodzapangira zinthu zakopa, zitsulo zodzapangira zinthu zachitsulo+ ndi matabwa+ odzapangira zinthu zamatabwa. Ndaperekanso miyala ya onekisi, miyala yomanga ndi simenti, miyala yokongoletsera, miyala yamtengo wapatali yamitundu yonse ndiponso miyala yambiri ya alabasitala. 3 Komanso chifukwa chakuti ndikusangalala ndi nyumba ya Mulungu wanga,+ kuwonjezera pa zonse zimene ndakonzekera zokhudza nyumba yopatulikayo, ndikupereka kunyumba ya Mulungu wanga chuma changa+ chomwe ndi golide ndi siliva. 4 Ndikupereka matalente* 3,000 a golide wa ku Ofiri,+ matalente 7,000 a siliva woyengedwa bwino wodzakutira makoma a nyumba,
-