Deuteronomo 32:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Yesuruni* atanenepa, anapandukira mbuye wake. Iwe wanenepa, wakula thupi, wakhuta mopitirira muyezo.+ Choncho iye anasiya Mulungu amene anamupanga,+Ndipo ananyoza Thanthwe la chipulumutso chake. 2 Mbiri 26:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Komanso Uziya anali ndi gulu la asilikali okonzeka kumenya nkhondo. Iwo ankapita kunkhondo mʼmagulumagulu. Asilikaliwa anawerengedwa komanso kulembedwa mayina+ ndi Yeyeli mlembi+ ndiponso Maaseya womuthandiza wake. Awiriwa ankayangʼaniridwa ndi Hananiya mmodzi wa akalonga a mfumu. 2 Mbiri 26:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unayamba kudzikuza mpaka kufika pomʼpweteketsa. Iye anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita mʼkachisi wa Yehova kukapereka nsembe zofukiza paguwa lansembe.+
15 Yesuruni* atanenepa, anapandukira mbuye wake. Iwe wanenepa, wakula thupi, wakhuta mopitirira muyezo.+ Choncho iye anasiya Mulungu amene anamupanga,+Ndipo ananyoza Thanthwe la chipulumutso chake.
11 Komanso Uziya anali ndi gulu la asilikali okonzeka kumenya nkhondo. Iwo ankapita kunkhondo mʼmagulumagulu. Asilikaliwa anawerengedwa komanso kulembedwa mayina+ ndi Yeyeli mlembi+ ndiponso Maaseya womuthandiza wake. Awiriwa ankayangʼaniridwa ndi Hananiya mmodzi wa akalonga a mfumu.
16 Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unayamba kudzikuza mpaka kufika pomʼpweteketsa. Iye anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita mʼkachisi wa Yehova kukapereka nsembe zofukiza paguwa lansembe.+