-
1 Mafumu 15:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Beni-hadadi anamvera Mfumu Asa ndipo anatumiza akuluakulu a asilikali ake kuti akamenyane ndi anthu amʼmizinda ya Isiraeli. Iwo analanda Iyoni,+ Dani,+ Abele-beti-maaka ndi Kinereti yense komanso dera lonse la Nafitali. 21 Basa atamva zimenezi, nthawi yomweyo anasiya kumanga Rama* ndipo anapitiriza kukhala ku Tiriza.+ 22 Ndiyeno Mfumu Asa inaitanitsa Ayuda onse moti palibe amene anatsala, ndipo iwo anatenga miyala ndi matabwa za ku Rama zimene Basa ankamangira. Mfumu Asa anatenga zinthu zimenezi nʼkukamangira mzinda wa Geba+ ku Benjamini ndi wa Mizipa+ kuti mizindayi ikhale yolimba.
-