6 Ndiye lamulani anthu anu kuti andidulire mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+ Antchito anga azidzagwira ntchito limodzi ndi antchito anu ndipo ndidzalipira antchito anu mogwirizana ndi malipiro amene munganene. Inuyo mukudziwa kuti pakati pathu palibe odziwa kudula mitengo ngati Asidoni.”+