-
Deuteronomo 4:41-43Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
41 Pa nthawi imeneyo, Mose anapatula mizinda itatu mbali yakumʼmawa kwa Yorodano.+ 42 Ngati munthu wapha mnzake mwangozi ndipo sanayambe wadanapo naye,+ munthu ameneyu azithawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti akhale ndi moyo.+ 43 Mizinda yake ndi Bezeri,+ mʼchipululu chimene chili mʼdera lokwererapo, woti anthu a fuko la Rubeni azithawirako. Mzinda wa Ramoti+ ku Giliyadi, woti anthu a fuko la Gadi azithawirako ndi mzinda wa Golani+ ku Basana, woti anthu a fuko la Manase+ azithawirako.
-