-
Oweruza 20:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Pakati pa asilikali amenewa, panali amuna amanzere 700 osankhidwa mwapadera. Aliyense wa amuna amenewa ankatha kuponya mwala nʼkugenda tsitsi limodzi osaphonya.
-
-
1 Mbiri 12:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Awa ndi anthu amene anapita kwa Davide ku Zikilaga+ pa nthawi imene iye sankayenda momasuka chifukwa choopa Sauli+ mwana wa Kisi. Iwowa anali ena mwa asilikali amphamvu amene anamuthandiza pankhondo.+ 2 Amuna amenewa anali onyamula mauta ndipo ankatha kugwiritsa ntchito mkono wamanja ndi wamanzere+ poponya miyala ndi gulaye+ kapena poponya mivi ndi uta. Amenewa anali abale ake a Sauli, a fuko la Benjamini.+
-