-
Ezara 4:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Mawu amene analembedwa mʼkalata ya mfumu Aritasasita anawerengedwa pamaso pa Rehumu, Simusai mlembi ndi anzawo. Kenako iwo anapita msangamsanga kwa Ayuda ku Yerusalemu nʼkukawaletsa ntchitoyo mwankhondo. 24 Pa nthawi imeneyi mʼpamene ntchito yomanga nyumba ya Mulungu, imene inali ku Yerusalemu, inaima ndipo inaima choncho mpaka chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo mfumu ya Perisiya.+
-