9 Zimenezi zitangotha, akalonga anabwera kwa ine nʼkundiuza kuti: “Aisiraeli, ansembe ndiponso Alevi sanadzipatule kwa anthu a mitundu ina komanso ku zonyansa za mitunduyo.+ Anthu ake ndi Akanani, Ahiti, Aperezi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aiguputo+ ndi Aamori.+