9 Choncho Yesuwa, ana ake ndi abale ake, Kadimiyeli ndi ana ake, ndi ana a Yuda,* ananyamuka mogwirizana kuti akayangʼanire anthu ogwira ntchito mʼnyumba ya Mulungu woona. Panalinso ana a Henadadi,+ ana awo ndi abale awo, omwe anali Alevi.
24 Atsogoleri a Alevi anali Hasabiya, Serebiya ndi Yesuwa+ mwana wa Kadimiyeli.+ Ndipo abale awo ankaima moyangʼanizana nawo nʼkumatamanda ndi kuyamika Mulungu mogwirizana ndi malangizo a Davide,+ munthu wa Mulungu woona. Gulu lililonse la alonda linaima moyandikana ndi gulu lina la alonda.