-
Ezara 7:14-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Iwe watumizidwa ndi mfumu komanso alangizi ake 7 kuti ukafufuze ngati anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu akutsatira Chilamulo cha Mulungu wako, chimene uli nacho.* 15 Utenge siliva ndi golide zimene mfumu ndi alangizi ake apereka mwakufuna kwawo kwa Mulungu wa Isiraeli, amene amakhala ku Yerusalemu. 16 Utengenso siliva ndi golide yense amene ulandire* mʼchigawo chonse cha Babulo, limodzi ndi mphatso za anthu komanso za ansembe omwe akupereka mwakufuna kwawo kunyumba ya Mulungu wawo, yomwe ili ku Yerusalemu.+
-