-
Ekisodo 2:23-25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Patapita nthawi yaitali mfumu ya Iguputo inamwalira.+ Koma Aisiraeli anapitirizabe kuvutika chifukwa cha ukapolo ndipo ankalira modandaula. Iwo anapitirizabe kulirira Mulungu woona+ kuti awathandize chifukwa cha ukapolowo. 24 Patapita nthawi, Mulungu anamva kubuula+ kwawo ndipo anakumbukira pangano lake ndi Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.+ 25 Choncho Mulungu anayangʼana Aisiraeli ndipo anaona mmene ankavutikira.
-