-
1 Mafumu 11:1-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Mfumu Solomo inakondanso akazi ena ambiri a mitundu ina+ kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao.+ Inakonda akazi a Chimowabu,+ a Chiamoni,+ a Chiedomu, a Chisidoni+ ndi a Chihiti.+ 2 Akaziwa anali ochokera mʼmitundu imene Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Musamakwatirane nawo komanso musamacheze nawo, chifukwa adzapotoza mitima yanu kuti muzitsatira milungu yawo.”+ Koma Solomo ankakonda anthu amenewa ndipo sanafune kuwasiya. 3 Iye anali ndi akazi olemekezeka 700 komanso akazi ena apambali 300 ndipo patapita nthawi, akaziwo anapotoza mtima wa Solomo.* 4 Iye atakalamba,+ akazi akewa anapotoza mtima wake moti Solomo ankatsatira milungu ina+ ndipo sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu ngati mmene anachitira bambo ake Davide. 5 Solomo anayamba kutsatira Asitoreti,+ mulungu wamkazi wa Asidoni ndi Milikomu,+ mulungu wonyansa wa Aamoni.
-