33 Pa tsiku la 4 tinayeza siliva, golide ndi ziwiya zija mʼnyumba ya Mulungu wathu.+ Titatero tinapereka zinthuzo kwa Meremoti+ mwana wa Uliya wansembe, yemwe anali limodzi ndi Eliezara mwana wa Pinihasi. Analinso limodzi ndi Yozabadi+ mwana wa Yesuwa ndi Nowadiya mwana wa Binui,+ omwe anali Alevi.