-
Yobu 1:6-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Tsopano linafika tsiku limene ana a Mulungu woona*+ anapita kukaonekera pamaso pa Yehova,+ ndipo Satana+ nayenso anafika pakati pawo.+
7 Kenako Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi ukuchokera kuti iwe?” Satanayo anayankha Yehova kuti: “Ndimazungulira mʼdziko lapansi komanso kuyendayendamo.”+ 8 Ndiyeno Yehova anafunsanso Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu? Padziko lapansi palibe wina wofanana naye. Iye ndi munthu wokhulupirika amene amachita zoyenera,*+ amaopa Mulungu ndiponso amapewa zoipa.”
-