11 Inetu ndimadikira kuti inu mumalize kulankhula.
Ndakhala ndikumvetsera mfundo zanu+
Pamene mumafufuza zoti munene.+
12 Ndakhala ndikukumvetserani mwachidwi,
Koma palibe aliyense wa inu amene wapereka umboni wosonyeza kuti Yobu ndi wolakwa
Kapena kuyankha zonena zake.