-
Ekisodo 14:21, 22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza panyanja,+ ndipo Yehova anachititsa kuti mphepo yamphamvu yakumʼmawa igawe nyanjayo usiku wonse nʼkuumitsa pansi pake.+ Choncho madziwo anagawanika.+ 22 Zitatero Aisiraeli anadutsa pakati pa nyanja, panthaka youma,+ madziwo ataima ngati khoma kudzanja lawo lamanja ndi lamanzere.+
-