33 Pambuyo pake, anatembenuka nʼkulowera Njira ya ku Basana. Ndiyeno Ogi+ mfumu ya ku Basana anabwera limodzi ndi anthu ake onse kudzamenyana nawo ku Edirei.+
8 Pa nthawi imeneyo tinalanda dziko la mafumu awiri a Aamori+ amene ankakhala mʼdera la Yorodano, kuyambira mʼchigwa cha Arinoni* mpaka kuphiri la Herimoni.+
10 Tinalanda mizinda yonse yakudera lokwererapo, mʼGiliyadi monse, mʼBasana monse, mpaka ku Saleka ndi ku Edirei,+ mizinda imene inali mu ufumu wa Ogi ku Basana.