20 Ndikadzawalowetsa mʼdziko limene ndinalumbira kwa makolo awo,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ ndipo akadzadya nʼkukhuta, zinthu nʼkuyamba kuwayendera bwino,+ adzatembenukira kwa milungu ina nʼkuyamba kuitumikira. Iwo adzandichitira mwano komanso kuphwanya pangano langa.+